Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 317

Paphata pa Chichewa Pachiindeinde: Pamponachimera, zafika posangalatsa. Chitsanzo: Msonkhanowo utafika pachiindeinde, pulezidenti anayamba kudikula. Pachika: (a) Kuulula zolakwa za wina, kuika munthu wina m’mavuto. Chitsano: Apa ndiye mwandipachikatu, zoona osan- goyankha zokhazo zomwe munafunsidwa! (b) Kusiya kugwiritsa ntchito chinthu. Chitsanzo: Njinga ija tinapachika. Pachimake: Pampondachimera, zafika posangalatsa. Chitsanzo: Ndimapita dansi ikafika pachimake. Pachiswe: Pangozi. Chitsanzo: Moyo wawo uli pachiswe. Padzuwa: Panjala, pamavuto. Chitsanzo: Anangotithawa n’kutisiya padzuwa. Paka chipere: Namiza. Chitsanzo: Amakuuzani kuti anayamba ntchito? Amaku- pakani chipere ndithu! Paka mafuta pakamwa: Kuchita chinyengo pofuna kupangitsa ena kuganiza kuti wachitira munthu zinazake. Chitsanzo: Angotipakapaka mafuta pakamwa, kuti azunguwa aziona ngati amatithandizadi. Paka munthu wina: Kunamizira munthu wina wosala- kwa. Chitsanzo: Anapereka mimba ndi wina koma iyeyo anan- gomupaka. Pakalapakala: Kuchita zinthu mofulumira, kumangogwiragwira zinthu. Chitsanzo: Ndinawapeza ali pakalapakala kukonzekera ulendo. 316