Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 315

Paphata pa Chichewa Onetsa zakuda: Menya kwambiri. Chitsanzo: Mukachita masewera akuonetsani zakuda. Ongaza: (a) Wamisala. Chitsanzo: Bambo aja ndi ongaza. (b) Wachamba. Chitsanzo: Mkulu ameneyu akuoneka kuti wangaza. Ongolani pakamwa: Lankhulanipo. Chitsanzo: Musangoti du, nanunso taongolaniko pa- kamwa. Opanda pake: Wosathandiza. Chitsanzo: Anthu amenewa ndi opanda pake, sangatithandize. Opanda pokopera: Anthu oipa, opanda pabwino. Chitsanzo: Anthu amenewa ndi opanda pokomera. Osainunkha: Osadya nawo kapena kulawa. Chitsanzo: Ukapanda kugwira ntchito suinunkha nsima lero! Osakaza: Owononga zinthu. Chitsanzo: Anthu amenewa ndi osakaza chakudya. Osalungama: Anthu oipa, ochita zimene Mulungu amadana nazo. Chitsanzo: Anthu osalungama sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu. Osamanditola: Kumandilemekeza, kumandipatsa ulemu. Chitsanzo: Osamanditola ayi, ndidzakuonetsani polekera. Osamandizolowera: Kumandilemekeza, kumandpatsa ulemu. Chitsanzo: Osamandizolowera ayi, ndidzakuonetsani polekera. Osamba: Apantchito, ophunzira, olemera. Chitsanzo: Akazi amasiku ano akumakhala osamba. 314