Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 31

Paphata pa Chichewa Chidani cha mphaka ndi khoswe: Udani waukulu kwambiri.f Chitsanzo: Azikazi awo ali paudani wa mphaka ndi khoswe. Chidikhodikho: Ntchirichiri, phokoso limene limachitika pakhosi. Chitsanzo: Munthu akatsala pang’ono kufa amapanga chidikhodikho. Chidima: Kulephera kuona bwinobwino kapena kuzindikira. Chitsanzo: (1) Ndimaona chidima chifukwa cha njala. (2) Ukaledzera thupi limachita chidima. Chidindiri: Wodziwa ntchito komanso yemwe wakhalitsa pantchito. Chitsanzo: Ameneyu ndiye chidindiri cha pakampani pano. Chidodo: (a) Kuchedwa. Chitsanzo: Mukamachita chidodo mutaya zambiri. (b) Kuyankhula mododoma, chibwibwi. Chitsanzo: Amachita chidodo poyankhula. Chidule: Kuchita zinthu mosalongosoka, kuchita zinthu mosazungulira. Chitsanzo: (1) Ntchitoyi usaigwire mwachidule. (2) Ndidutsa njira yachidule. Chidyamakanda: Munthu wokonda kuchita zachiwerewere ndi ana kapena anthu omwe si a msinkhu wake makamaka aang’ono kwa iyeyo. 30