Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 306
Paphata pa Chichewa
Nthyole: Chikwapu.
Chitsanso: Mwana wamwano amakhala bwenzi la nthyole.
Ntibu: Wailesi.
Chitsanzo: Agula ntibu.
Ntolo: Mavuto, mulu womangidwa pamodzi wa nkhuni.
Chitsanzo: (1) Ndani angatitule ntolowu! (2) Wasenza ntolo
wankhuni.
Ntopola: Mwano, zachipongwe.
Chitsanzo: Akapitirizabe kuchita zantopola amenyedwa.
Nunkha chitonde: Kununkha thukuta ngati mmene
mbuzi yaimuna imachitira. Zimakonda kuchitikira amu-
na.
Chitsanzo: Nditalikire, ukununkha chitonde!
Nyala:
(1) Kuchita manyazi.
Chitsanzo: Namwali ayenera kunyala akakumana ndi
mwamuna.
(b) Kudikira nthawi yaitali.
Chitsanzo: Mudikirira mpaka kunyala.
Nyambita mapazi a munthu: Nyengerera.
Chitsanzo: (1) Kuteroko anabweranso kudzakunyambitani
mapazi. (2) Kuti andithandiza akufuna ndichite kuwan-
yambita mapazi.
Nyambita mwana (munthu): Kulekerera mwana, kulera
mwana momunyengerera.
Chitsanzo: Anakula mopulukira chifukwa makolo awo
ankawanyambita.
Nyambitana: Kukondana kwambiri.
Chitsanzo: Banja limene lija limachita kunyamitana.
Nyambo m’masiku: Lidzafika tsiku lake.
Chitsanzo: Asiyeni, nyambo m’masiku. Adzatifuna!
305