Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 303

Paphata pa Chichewa yolimba ngati imeneyi. (2) Anazolowera kugwira ntchito yolimba. Ntchito yowawa (ntchito yopweteka): Ntchito yomwe susangalala kuigwira chifukwa umavutika nayo kapena ndi yofuna mphamvu kwambiri. Chitsanzo: Amagwira ntchito yowawa tsiku lonse. Ntchona: Munthu yemwe anachoka kwawo n’kukakhazi- kika kwinakwake. Nthawi zinanso angatanthauze munthu amene amachita zautambwali. Chitsanzo: Ameneyu ndi ntchona ya m’tauni muno. Nthabwala: (a) Nkhani zoseketsa anthu. Chitsanzo: Achimwene anu ndi a nthabwala. (b) Wokonda zoseka. Chitsanzo: Amalume ndi anthabwala. Nthabwala: Wokonda kukamba nkhani zoseketsa. Chitsanzo: (1) Bambowa ndi anthabwala. (2) Ndinamupeza akunena nthabwala. Nthambo: (a) Chingwe kapena waya wantali. Chitsanzo: Ndani wamangirira nthambo yake apa? (b) Mwado, panti. Chitsanzo: Zoona mungayanike nthambo zanu pachingwe? Nthanda: Munthu wokongola kwambiri. Chitsanzo: Achiredzerere aja anakwatira kanthanda ka pantundapo. Nthata: Wokakamira. Chitsanzo: Mnyamata ameneyu ndi nthata eti, monse ndayambira kumukana muja! Nthawi yabwino: Nthawi yoyenera kuchita zinthu, nthawi yopanda mavuto. Chitsanzo: Imeneyi ndi nthawi yabwino yoyamba kulima. 302