Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 300
Paphata pa Chichewa
Chitsanzo: Anamalira onse anamanga nsangamutu.
Nsanje:
(a) Mtima wosafuna kuti wina zizimuyendera.
Chitsanzo: Munthu ameneyu amandichitira nsanje.
(b) Kusafuna kuti munthu wina azicheza ndi mwamuna
kapena mkazi wako.
Chitsanzo: Atelala mundilinge ndi maso, amunanga
nsanje!
Nsanza zokhazokha: Usiwa.
Chitsanzo: Mukuseweretsa ndalama apa, chonsecho ma-
kolo anu ali nsanza zokhazokha.
Nsapule: Ndolo zovala m’makutu.
Chitsanzo: Nduke zenizeni zimatchena nsapule.
Nsasa: Kanyumba komangidwa ndi udzu. Nthawi zina an-
thu amanena dzinali akamatchula nyumba yawo kapena
kumene amakhala.
Chitsanzo: (1) Amanga misasa yoti achitireko chinamwali.
(2) Kameneka ndiye kansasa kathu.
Nsatsi: Mafuta ochokera ku zitsamba zinazake.
Chitsanzo: Kale anthu ankadzola mafuta a nsatsi.
Nseko: Kasekedwe, kuseka.
Chitsanzo: (1) Ndinadziwa kuti nseko umenewo ndi wa
achimwene. (2) Amakamba nkhani zokodola nseko.
Nsengwa: Lichero, lisero, thunga.
Chitsanzo: Mubweretse kansengwa kuti titengeromo
masamba.
Nsenye: Mwana wongobadwa n’kupitirira.
Chitsanzo: Munthu yemwe sakhutitsidwa ndi zimene ali
nazo amaposedwa ndi nsenye.
Nsima tepetepe (teputepu): Nsima yosalimba.
Chitsanzo: N’chifukwa chiyani waphikanso nsima ya
tepetepe (teputepu).
299