Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 281
Paphata pa Chichewa
Mzamba: Munthu wothandiza azimayi pobereka.
Chitsanzo: Mādziko muno muli azamba ochepa.
Mzime: Munthu womalizira kubadwa.
Chitsanzo: Ine ndinadziwa kuti ndi mzime nditaona
zimene ankachita. Zikuoneka kuti anamulerera pachilolo.
Mzinda:
(a) Malo ochitira chinamwali.
Chitsanzo: Kumzinda sikuyenera kufika anthu
osavinidwa.
(b) Tauni.
Chitsanzo: Mzinda wa Lilongwe ndi wosalongosoka.
Mzozodo: Alibe munthu wopikisana naye.
Chitsanzo: Sungakhale mzozodo pa chilichonse.
280