Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 28
Paphata pa Chichewa
Chera nkhoko: Kuchenjera udakali mwana wamng’ono.
Chitsanzo: Ana ambiri masiku ano akumachera nkhoko.
Chesula: Mawu amenewa amagwiritsidwa ntchito ponena
za zikhulupiriro zomwe anthu a ku Africa kuno amakhala
nazo zoti anthu amatha kulodzana.
Chitsanzo: N’chifukwa chiyani wayamba kuyenda usiku,
akuchesula eti?
Cheuka:
(a) Yang’ana kumbuyo.
Chitsanzo: Akamayenda sacheuka.
(b) Kuona chimene chakuthandiza.
Chitsanzo: Ukapulumuka m’mavuto umafunika
kumacheuka, n’kuona chakuthandiza.
Chibaba: Kufunitsitsa kuchita chinachake chomwe
unazolowera.
Chitsanzo: (1) Ali ndi chibaba cha fodya. (2) Wapeza
namwali kuti azidzachengetera chibaba chake.
Chibadwire: Osavala.
Chitsanzo: (1) Akumazungulira nyumba usiku ali
chibadwire. (2) Ngati masitailo sasintha, zaka zikubwerazi
anthu azidzangoyenda chibadwire.
Chibakera: Khofi.
Chitsanzo: Anawamenya chibakera.
Chibale chokumba: Chibale chapatali kwambiri.
Chitsanzo: Chibale amachikokomezachotu ndi chokumba.
Chibalo: Ntchito yopweteka, chilango.
Chitsanzo: Amupatsa chibalo choti aime mwendo umodzi
mpaka aphunzitsi atuluke m’kalasi.
27