Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 274
Paphata pa Chichewa
Munthu wowola m’kamwa: Wotukwana.
Chitsanzo: Sitifuna anthu owola m’kamwa,
angationongere ana pakhomo pano.
Munye kupala champhongo: Wamng’ono woposa
wamkulu, monga ana ang’onoang’ono ali ndi ana, pomwe
akulu alibe.
Chitsanzo: Nthumbidwa zonse timazinyamula
pamiyendozi, zasanduka makolo. Ndithu munye kupala
champhongo.
Muphulika maso: Muona zosaona.
Chitsanzo: Usayang’ane ungaphulike maso.
Musandipomboneze: Musandisokoneze.
Chitsanzo: Musandipomboneze inu, mukuti wapita
kumsika pomwe ndakumana naye kuseliku?
Mutu umodzi: Munthu m’modzi, wekhawekha.
Chitsanzo: (1) Mutu umodzi sungalimbane ndi mavuto
amenewa. (2) Vuto limeneli likufuna anthu angapo, osati
mutu umodzi.
Mutu wa banja: Mwamuna.
Chitsanzo: Mutu wa banja ndi amene ayenera kupezera
ana zosowa za pamoyo wawo.
Mutu wake umakoka: Mutu wake umagwira.
Chitsanzo: Mwanayu mutu wake umakoka.
Mutu wandikula kapena wandilemera: Kusowa chochita.
Chitsanzo: Vutoli lakula ndipo mutu wandilemera
(wandikula).
Mutu: Mowa woyamba kutchezedwa.
Chitsanzo: Ndinadziwa zoti mayi amene aja aukazinga
nditalawa mutu wa kachaso yemwe anatcheza dzulo.
Muyeso (muyezo): Choyezera.
Chitsanzo: Muyeso uli kuti?
273