Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 272
Paphata pa Chichewa
Mudzi:
(a) Manda, nthumbira.
Chitsanzo: Mupite ndi awa akakulozereni mudzi umene
achimwene anu anagona.
(b) Matenda otupa maliseche, ena amati mdidi. Matenda-
wa amakonda kugwira amuna.
Chitsanzo: Akuvutika ndi mudzi.
Mudzi: Manda
Chitsanzo: Adzukulu atamaliza kukumba mudzi woti aike
malirowo, anangoona kwatulikira chinjoka, moti onse
analikumba liwiro.
Muisova: Popeza mwadziwa izizi, muona zimene
mungachite. Mawuwa anachokera kuchingerezi.
Chitsanzo: Popeza mwamva, muisova.
Mukadayenda: Mukadali ndi moyo.
Chitsanzo: (1) Ndi bwino mukonze tsogolo la ana anu
mukadayenda. (2) Ndinali munthu ine agogo akadayenda.
Mulu: Zinthu zounjikana.
Chitsanzo: (1) Ali ndi mulu wa ndalama. (2) Ndani waun-
jika mulu wamanyiwu?
Mumphipi: M’mbali.
Chitsanzo: Akufuna matabwa a mphipi zazikulu.
Mumpoto mosapita therere: Amangodyera nyama, sa-
konda masamba.
Chitsanzo: Mayiwa ndi a dovu, mpoto mwake simupita the-
rere.
Munali kale: Zinkakuyenderani kale, munatha inu.
Chitsanzo: Munali kale inu, ndalama zikukuyanjani.
Munasamba pati? Mawuwa amatanthauza kuti chinsinsi
chanu ndi chani?
Chitsanzo: Munasamba pati anzathu kuti zizikuyenderani
chonchi?
271