Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 265
Paphata pa Chichewa
Mphitapansi: Wochita chiwembu mobisalira.
Chitsanzo: Simumadziwa kuti amene uja ndi
mphitapansi?
Mphulupulu: Kusamvera, kuvuta.
Chitsanzo: Mwana wanuyu ndi wamphulupulu.
Mphumi: Mwayi.
Chitsanzo: Amene achita mphumi ndi a Nasimango.
Mphungusatayanthenga: Munthu womana kwambiri
kapena woumira. Mphungu ndi mbalame yomwe
imauluka m’mwamba kwambiri ndipo nthenga yake
ikathothoka, imaiwakha isanafike pansi.
Chitsanzo: (1) Zakudya zawotu amadyera mugombeza.
Amene aja ndi mphungusatayanthenga. (2) Mwanuna
wawo ndi phungusatayamthenga.
Mphuno bii: Mawu achipongwe onena za munthu yemwe
simukufuna mutamuona.
Chitsanzo: Tamuonani, ali mphuno bii, kaya wabwera
kudzatani?
Mphuno zipida: Pang’ono kwambiri.
Chitsanzo: Ndinamutuma kuti akatenge zonse, koma
anangonditengera mphuno zipida.
Mphuno: Kakang’ono.
Chitsanzo: Ndinamutuma kuti akatenge zonse, koma
anangonditengera mphuno.
Mphwanga: Mng’ono wanga.
Chitsanzo: Uyu ndi mphwanga.
Mphwayitolo: Waulesi, munthu womati chioneke chion-
eke.
Chitsanzo: Kukacha koma kuothera dzuwa, mukamuuza
kuti akalime amanamizira kudwala. Amene uja ndi
mphwayitolo.
Mphwephwa:
(a) Munthu wopanda mphamvu.
264