Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 261

Paphata pa Chichewa ndikuwayang’anira azichita zinthu mosalongosoka. Mosapumira: Mosalekeza. Chitsanzo: Amangwira ntchito mosapumira. Mosataya nthawi: Mofulumira. Chitsanzo: Kumachita zinthu mosataya nthawi. Mosayang’ana nkhope: (a) Mopanda chisoni. Chitsanzo: Akhoza kukumenya mosayang’ana nkhope. (b) Mosakondera. Chitsanzo: Amathandiza aliyense mosayang’ana nkhope. Motayirira: Mosadzilemekeza, monyanyira. Chitsanzo: Azimayi ena amavala motayirira. Mothinana: Mopanikizana kwambiri. Chitsanzo: (1) Akaidi amakhala mothinana. (2) M’munda mwawo muli nthochi zothinana. Mothithikana: Mopanikizana kwambiri. Chitsanzo: M’kalasi yathu timakhala mothithikana Moto wolusa: Moto woopsa kwambiri, wamphamvu. Chitsanzo: Moto wolusa waotcha nsika. Moto: (a) Mawu amene amagwiritsidwa ntchito pouzae ena kuti anyamuke kapena apitirize. Munthu angathenso kutchula mawuwa ponena kuti akunyamuka kapena akupitiriza. Chitsanzo: Bwanayo atakwera galimotoyo, anauza dalaiva wake kuti, “Moto!” (b) Munthu wonyankhulayankhula kapena wolongolola. Chitsanzo: Mkazi amene anakwatira uja ndi moto. Motomoto: (a) Mawuwa amanenedwa ngati wina zinthu zikumuyen- dera kapena ngati akumadya wani m’mudzi kapena pa- malo. Chitsanzo: Mnyamata amene uja ndi motomoto. 260