Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 26

Paphata pa Chichewa Chamtengo wapatali: Chodula, cha ndalama zambiri. Chitsanzo: Sindingakwanitse kugula chinthu chamtengo wapatali ngati chimenechi. Chamuna (chimuna): Mphamvu. Chitsanzo: Kuti unyamule thumbali mpofunika chamuna. Changamuka: Chenjera. Chitsanzo: Tikufuna munthu wochangamuka. Changamutsa: Chenjeretsa, kupusitsa, kukubera munthu. Chitsanzo: (1) Kanyamulidwe kake kameneka akuchangamutsani akuba. (2) Munotu ndi m’tauni, mukagona pang’ono akuchangamutsani. Changu pamalo: Ndi bwino kumachita zinthu mwachangu. Chitsanzo: Tiyeni tipange changu pamalo. Chaomba mtengo n’chomwecho: Zigwezo n’zomwezo. Chitsanzo: Masiku ano tikungokhalira kupirira, chaomba mtengo n’chomwecho. Chapa: Kumenya kapena kumenyedwa kwambiri. Chitsanzo: (1) Sakupeza bwino, anzake anamuchapa koopsa. (2) Mwana amene uja ndidzamuchapa tsiku lina. Chapamwamba: (a) Chinthu chodula. Chitsanzo: Wagula wailesi yapamwamba. (b) Chinthu kapena ntchito yabwino kwambiri. Chitsanzo: Amagwira ntchito yapamwamba. 25