Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 249
Paphata pa Chichewa
kumeneko, mbuzi ikakonda, amalonda ali pafupi.
Mbuzi: Mawuwa amanena za munthu wosamva. Angatan-
thauzenso chiweto cha mbuzi.
Chitsanzo: (1) Mwana uyu ndi mbuzi! (2) Pamalilowo ma-
fumu ambiri anapereka mbuzi. Yemwe amalengeza zime-
nezi atatopa kunena kuti amfumu akutiakuti apereka
mbuzi, anayamba kumangonena kuti amfumu akuti,
mbuzi. Amfumu akuti, mbuzi, moti anthu amaona ngati
akunyoza mafumu.
Mbuzi: Munthu wosamva.
Chitsanzo: Iweyo ndiwe mbuzi, suumvayi.
Mbuzitchire: Nyani. Mawu onena mwachining’a omwe
ena amagwiritsa ntchito ponena za nyani. Amagwiritsa
ntchito mawu amenewa akamafuna kumupanga ndiwo.
Nanga aipe ndi dzina lomwe, bola kumupatsa lodyera.
Chitsanzo: Lero aphika mbuzitchire.
Mbwembwembwe: Zambirimbiri.
Chitsanzo: (1) Nsalu mukufunazo zangati mbwembwemb-
we. (2) Ngumbi zangoti mbwembwembwe.
Mbwembwezera: Nyenyerera, kutaya pansi.
Chitsanzo: Ndani amambwembwezera madeya apa?
Mbwita: Kulephera kugwira kapena kupeza chinthu.
Chitsanzo: (1) Amene wambwita adya mbewa yomwe
wathawitsayo. (2) Anaponya bwino nkhwangwayo, koma
wambwita.
Mchikumbe: Munthu wolima kwambiri.
Chitsanzo: Mchikumbe weniweni amayamba kulima
akangomaliza kukolola.
Mchimba (michimba): Manyi ouma.
Chitsanzo: Agalu aunjika michimba kuseliko.
Mchira wakhoswe: Chinthu chosachedwa kutha monga
chuma.
248