Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 246
Paphata pa Chichewa
mayi akunyumba ngati kuti pali ena akunjira.
Chitsanzo: Amenewa ndiye mayi akunyumba.
Mazangazime: Mavuto osaneneka, khaulitsa.
Chitsanzo: Akabweranso mowa uli m’mutu ndimuonetsa
mazangazime.
Mazangazime: Zoopsa.
Chitsanzo: Anthu olusa amuonetsa mazangazime.
Mazenene: Kusamveka bwino, kumveka modukaduka.
Chitsanzo: (1) Mawu anu akumveka mazenene lero. (2)
Wailesiyi ikumveka mazenene.
Mazenene: Kusamveka bwino.
Chitsanzo: (1) Wailesiyi ikumveka mazenene. (2) Mawu
awo amamveka mazenene.
Maziko:
(a) Pansi penipeni pa chinthu.
Chitsanzo: Maziko a nyumbayi ndi osalimba.
(b), pamene nkhani kapena chinthu chachokera.
Chitsanzo: Mpofunika tipeze maziko a nkhaniyi.
(c), kumanga nyumba.
Chitsanzo: Abale anu aja anamanga maziko m’taunimu.
Mazoba: Chichewa cha achinyamata chotanthauza
amuna kapena anyamata.
Chitsanzo: Mazoba enaake amandipatsa moni ngati
anamva zoti ndimadya moni ine.
Mbadwa: Munthu wobadwira m’dziko kapena dera lina.
Chitsanzo: Ife ndi mbadwa za dziko la Malawi.
Mbalume: Mfundo zomveka bwino zomwe munthu
amanena pofuna kukopa wina.
Chitsanzo: Mnyamatayu ali ndi mbalume.
Mbalume: Mfundo.
Chitsanzo: (1) Akuluwa ali ndi mbalume. (2) Kufunsira ku-
mafuna munthu wambalume.
245