Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 238

Paphata pa Chichewa Mangawa: Kugonana muukwati. Chitsanzo: Akayambana, akazi awo akumawamana man- gawa. Mangitsa madzi m’masamba: Kumudikiriritsa munthu koma osabwera. Chitsanzo: Tinagwirizana kuti tikumane kumtsinje, koma nditafikako, ndinazindikira kuti wandimangitsa madzi m’masamba. Mangolomera: Mphamvu zambiri, kutemera mankhwala opangitsa kuti munthu akhale wamphamvu kwambiri. Nthawi zina amagwiritsidwa ntchito ponena za munthu amene wapezanso mphamvu. Chitsanzo: (1) Munthu ameneyu ndi wamangolomera. (2) Chigoli chimene anamwetsacho chinawapatsa mangolomera. Manja a kape (manja a sefa): Manja osasunga kathu. Chitsanzo: (1) Ali ndi manja a kape. (2) Ali ndi manja a se- fa. Manja atherere: Osachedwa kuswa zinthu. Chitsanzo: Musamupatse matambulawo ali ndi manja ath- erere. Manja lende: Ulesi. Chitsanzo: Mtsikanayu ndi wamanja lende. Manja: Munthu yemwe amati akabzala mbewu zimabereka bwino. Chitsanzo: (1) Onani maungu kukula ngati mutu wa munthu. Azakhalitu muli ndi manja abwino. (2) Agogo mudzale ndinu, muli ndi manja a maungu. Mankhwala achikuda: (a) Makhwala azitsamba, mankhwala omwe nthawi zambiri amakhala ndi zizimba zake. Amatha kukuuza kuti ukamwere m’chipande, ukamwere pakhomo kapena ukamwe utavula malaya. Amakhulupirira kuti akapanda 237