Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 235

Paphata pa Chichewa Makutu pekupeku: Munthu yemwe makutu ake amangokhala m’mwamba kuti akamva nkhani akaikhuthure kwina. Chitsanzo: Kunyumba kwathu kunabwera munthu wa makutu petupetu uja. Makwacha: Ndalama zambiri. Chitsanzo: Chaka chino ndipha makwacha. Malamulo achitsulo: Malamulo okhwima. Chitsanzo: Boma lakale lija linkakhazikitsa malamulo achitsilo. Malamulo okhwima: Malamulo ovuta kuwatsatira, malamulo okhala ndi chilango chopweteka. Chitsanzo: Anthu sakubanso chikhazikitsireni malamulo okhwima. Malango: Mwambo. Chitsanzo: Mupite naye kumudzi akamupatse malango. Malasankhuli: Mphalabungu, zinkhuwala. Chitsanzo: Tinadyera malasankhuli. Malata a pamutu: Dazi. Chitsanzo: Ana a masiku ano sakumachedwa kukhoma malata pamutu. Malemu: Munthu womwalira. Chitsanzo: Malemu amuna awo anawasiyira chuma. Malipiro: (a) Ndalama zomwe munthu amalandira akagwira ntchito. Chitsanzo: Ntchito yonse imene ndikugwirayi, malipiro ake angakhale amenewa! (b) Zotsatira za zimene wachita. Nthawi zambiri mawuwa amanenedwa ngati mkuluwiko munthu akakumana ndi zotsatira za zochita zake zoipa. Chitsanzo: Mimba watengayo ndi malipiro a uhule amachita uja. 234