Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 230
Paphata pa Chichewa
M’bandakucha: Mmawa kwambiri kusanache.
Chitsanzo: Tinyamuka m’bandakucha.
M’bedu: Chinagwa chokukuta.
Chitsanzo: Mukandigulireko m’bedu.
M’bindikiro (kubindikira): Kumangokhala m’nyumba
kapena malo enaake osatuluka.
Chitsanzo: (1) Anzanuwo ali pa m’bindikiro. (2) Mwanayu
amangobindikira m’nyumba.
M’bwaa: Nsapato.
Chitsanzo: Ndagula m’bwaa inayake motchipa.
M’kamwa mwa mbuzi: Zokwinyika. Mwina anthu
amanena zimenezi chifukwa cha mmene mbuzi imatafuni-
ra moti chinthu chimene chatuluka m’kamwa mwake
sichingakhale chowongoka.
Chitsanzo: Zovala zawo zikungokhala ngati zinali m’kam-
wa mwa mbuzi.
M’kamwam’kamwa: Aliyense kumangokamba zomwezo,
nkhani imene yafala.
Chitsanzo: Nkhani ili m’kamwam’kamwa ndi ya ukwati
wawo.
M’manja molakwika: Amanenedwa zinthu zikakhala kuti
zapezeka kwa anthu osayenera.
Chitsanzo: Zinthunzizi zikafika m’manja molakwika muk-
azipezera patali.
M’maso muli gwa! Mopanda manyazi.
Chitsanzo: Amawatukwana mayi ake m’maso muli gwa!
M’mbuyo mwa alendo: Kuchedwa, zinthu zitachitika
kale.
Chitsanzo: Pamene ankaganiza zoti anene chilungamo
munali m’mbuyo mwa alendo.
229