Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 226
Paphata pa Chichewa
Chitsanzo: Matenda aja angolowa libolonje moti tikukaiki-
ra ngati atachire.
(b) Kusokonekera, kuwonongeka, kuipiraipira, kufooka pa
makhalidwe.
Chitsanzo: (1) Sukulu yangolowa libolonje. (2) Dzikoli
langolowa libolonje.
Lowa m’chala: Kudwaladwala.
Chitsanzo: Agogo masiku ano alowa m’chala.
Lowa m’chikanamba: Chita manyazi.
Chitsanzo: Anandichititsa manyazi kwambiri moti
ndinangolowa m’chikanamba.
Lowa m’chipiringu: Kulowa m’gulu.
Chitsanzo: Anatizemba n’kulowa m’chipiringu ndipo
sitinamuonenso.
Lowa m’dzombe: Kulowa m’gulu.
Chitsanzo: Wakubayo ataona kuti anthu ayamba
kumuthamangitsa, anangolowa m’dzombe ndipo
sanaonekenso.
Lowa m’khutu (m’makutu): Sokosera.
Chitsanzo: (1) Tamuuzani ali panjayo akhale chete aku-
tilowa m’khutu (m’makutu). (2) Takhala chete ukutilowa
m’khutu iwe!
Lowa m’maso: Kusaona chinthu choti usankhe chifukwa
zonse ndi zooneka bwino.
Chitsanzo: Nsaluzi zandilowa m’maso, sindikuonapo
yabwino yoti ndingasankhe.
Lowa m’mimba (boola m’mimba): Kuvutitsa kwambiri,
kuopsezedwa.
Chitsanzo: Amanena zimenezi kuti angotiboola m’mimba.
Lowa m’thengo: Kuchita misala.
Chitsanzo: (1) Ukapitiriza kusuta chamba, ulowa m’then-
go. (2) Achimwene awo analowa m’thengo.
225