Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 215
Paphata pa Chichewa
Kuyenda:
(a) Kucheza kapena kugwirizana kwambiri ndi munthu.
Tanthauzo lenileni la mawuwa ndi kuchoka penapake
kupita kwina pogwiritsa ntchito miyendo.
Chitsanzo: Nanjekeya amayenda ndi Nasimango.
(b) Kukhala pachibwenzi ndi munthu wina.
Chitsanzo: Mtsikanayu amayenda ndi bambo awo!
Kuyendana m’mapazi: Kulondanalondana.
Chitsanzo: Sindikufuna zoyendana m’mapazi.
Kuyendana pansi: Kokonzerana chiwembu kapena
kukamba za anthu ena.
Chitsanzo: Zoona osandiuza kuti mukupita? Apatu ndiye
mwandiyenda pansi.
Kuyerekedwa: Kuchita matama, kuvuta.
Chitsanzo: Ambiri akalemera amayamba kuyerekedwa.
Kuyeserera: Kuchita zinazake pongokonzekera.
Chitsanzo: Ndisanasewere ndiyeserere kaye.
Kuyezimira (kuyayamira): Kuchita dzanzi kwa mano.
Chitsanzo: Ndikadya mango aawisi, mano anga amaye-
zimira.
Kuyezimira mano: Mano kuchita dzanzi.
Chitsanzo: Ndinadya mango aawisi moti mano anga
ayezimira.
Kuyimba sukulu: Kuphunzira sukulu.
Chitsanzo: Anyani anauza Sibo kuti akufuna kuimba
nawo sukulu.
Kuyoyoka thupi: Kuwonda.
Chitsanzo: Atangowapeza nako anayamba kuyoyoka thupi.
Kuyoyoka:
(a) Kugwera pansi nthawi imodzi.
Chitsanzo: Masamba ayoyokera pakhomo ponse.
214