Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 213
Paphata pa Chichewa
zikuvina. Ndinaona kuti ndindingapitirize kumvetsera za
kuntchini kwadzadza ngati zimenezi.
Kuyankhulira nsonga ya lirime: Kunyada.
Chitsanzo: Mkazi wake amayankhulira nsonga ya lirime.
Kuyankhulitsa pambali: Kuchititsa kuti munthu anene
zolakwika.
Chitsanzo: Usandiyankhulitse pambali wamva?
Kuyasamula (kuyadamula): Kutsegula kukamwa komwe
kumachitika munthu akatopa kapena akakhala kuti
sanadzuke bwino.
Chitsanzo: Akatopa amangoyasamula.
Kuyayamira (kuyezimira): Mano kuchita dzanzi.
Chitsanzo: Ndinadya mango aawisi moti mano ayayamira.
Kuyedzeka nzere: Kulima mnzere.
Chitsanzo: Ndikayedzeka mizere itatu ndizipita.
Kuyenda chikachika: Kuyenda movutikira.
Chitsanzo: Chigalimotocho chimayenda chikachika.
Kuyenda chinochino: Kuyenda osavala.
Chitsanzo: Ngati anthu akuvala chonchi masiku ano, zaka
zikubwerazi azidzayenda chinochino.
Kuyenda chogona: Kumwalira.
Chitsanzo: Ndikusowa mtengo wogwira kuona amalume
anga akuyenda chogona.
Kuyenda m’chigwa cha nthunzi wa imfa: Kutsala
pang’ono kumwalira.
Chitsanzo: Mudzandithandize ndikamadzayenda
m’chigwa cha nthunzi wa imfa.
Kuyenda malonda:
(a) Kukondedwa, kufunidwa ndi anthu ambiri.
Chitsanzo: Mtsikanayutu ndiye akuyenda malonda
masiku ano.
212