Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 203
Paphata pa Chichewa
Kutsinkha: Kudya ndiwo zokhazokha.
Chitsanzo: Anawa akutsinkha ndiwo.
Kutsira (kumwetsa): Kuchinya chigoli. Mawuwa amag-
wiritsidwa ntchito pa masewera a mpira wa miyendo.
Chitsanzo: Anyamata onse omwe anatsira (anamwetsa) zi-
goli anawapatsa mendulo.
Kutsitsa mpweya: Kuphwisa.
Chitsanzo: Ndani wopanda nzeru amena watsitsa mpweya
m’minibasi yopanda mawindo ngati ino!
Kutsogoza: Kupha.
Chitsanzo: Anakulakwirani chiyani kuti muwatsogoze
asanadyerere?
Kutsomphoka:
(a) Kuchoka mwamphamvu.
Chitsanzo: Lamba wa msamphawo anatsomphoka
n’kumukwapula miyendo.
(b) Kukula mofulumira.
Chitsanzo: Mwanayu ndiye watsomphokatu, chaka chatha
chomwechi anali wam’manja.
Kutsuka m’kamwa: Kudya zakudya zankhuli.
Chitsanzo: Tiphe nkhuku kuti titsukeko m’kamwa.
Kutsukunyula: Kukalipira.
Chitsanzo: Ngakhale mumutsukunyule sasintha.
Kutsungula: Kulemera, kukhala ndi moyo wabwino.
Chitsanzo: Anthu akusamuka m’mayiko osauka
n’kumapita kumayiko otsungula.
Kutsutsula pabala (pachilonda):
(a) Kukumbutsa mavuto omwe munthu anakumana
nawo.
Chitsanzo: Zimene akuchitsazi akungotitsutsula pabala.
(b) Kuputa munthu.
Chitsanzo: Anthu amenewa akunditsutsula pabala.
202