Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 193

Paphata pa Chichewa Kususuka: Kukhala wadyera. Chitsanzo: Bambowa ndi osusuka. Kuswa m’tu wangoma: Ulula zinthu zomwe munapangana kuti simuulura. Ubongo wa ngoma umakhala wowawa. Ndiye chimene chinachitika n’choti munthu wina ndi mnzake anapita kwinakwake komwe anamvako zachinsinsi ndipo anapangana kuti asaulule. Koma atafika, winayo anayamba kuswa mutu wa ngoma. Kuulula nkhani yowawa titero kunena kwake. Chitsanzo: Tinagwirizana kuti tisanene chilichonse. Koma titafika, anayamba kuswa m’tu wangoma. Kuswa mphanje: (a) Kuyamba kumene kuchita chinachake kapena kuyam- bitsa. Chitsanzo: Mukufuna kufunsira ndani? Tiuzeni tika- kuswereni mphanje. (b) Kuyamba kulima malo omwe sanalimidwepo. Chitsanzo: Chaka chino ndikufuna kuswa mphanje. Kuswa mtima: Kukhumudwitsa. Chitsanzo: Nkhaniyi yaswa mtima wanga. Kuswa mutu: Kuganiza kwambiri. Chitsanzo: (1) Masamu amafunika anthu omwe amaswa mutu kwambiri. (2) Nkhaniyi ndi yovuta zedi, yofunika kuswa mutu. Kuswa nthanga m’lichero: Ulula zinthu zomwe munapangana kuti simuulura. Chitsanzo: Tinagwirizana kuti tisanene chilichonse. Koma titafika, anayamba kuswa nthanga m’lichero. Kuswa: Kumenya. Chitsanzo: Ukachitanso zimenezi ndikuswa. Kuswaya: Kusiya kuwerengera munthu, kudana ndi munthu. Chitsanzo: (1) Atangolemera anawaswaya anzawo onse. (2) Anatiswaya atangosamuka kuno. 192