Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 190
Paphata pa Chichewa
(2) Mwana ameneyu amashupa kwabasi.
Kushupika: Kuvutika kwambiri.
Chitsanzo: Abale awo akushupika.
Kusinira: Kugwiritsa ntchito zinthu mosamala, kudya
pang’onopang’ono.
Chitsanzo: Ndiwo ndakupatsanizi muzisinira.
Kusinja mkonono: Kuliza mkonono kwambiri.
Chitsanzo: Mwana uyu amausinja mkonono.
Kusinja:
(a) Kulira bwino.
Chitsanzo: Wailesiyi ikusinja!
(b) Kuphwanya zinthu.
Chitsanzo: Sinjani chimangachi mumtondomo.
(c) Kumenya munthu.
Chitsanzo: Anzake amusinja koopsa.
Kusintha maganizo: Kusiya zimene amaganiza
n’kutsatira zina.
Chitsanzo: N’chifukwa chiyani mwasintha maganizo
achimwene?
Kusisima: Mawuwa amatanthauza kulira mwapansipansi
koma mopwetekedwa mtima. Koma angatanthauzenso
zinthu zoola, ena amati zoonongeka.
Chitsanzo: (1) Ndinawamva akusisima kuchipinda kwawo.
(2) Ndiwo zijatu zasisima.
Kusiya fumbi: Kuthawa.
Chitsanzo: Ataona kuti zavuta, mnyamatayo anasiya fum-
bi.
Kusiya gaga: Kumwalira.
Chitsanzo: Ukapitiriza khalidwe loipali usiya gaga.
Kusiya m’gaiwa (gaga): Mawu achipomwe onena za mun-
thu amene wamwalira.
Chitsanzo: (1) Chigawenga chija chasiya m’gaiwa (gaga).
(2) Ukapitiriza khalidwe loipali usiya m’gaiwa.
189