Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 187

Paphata pa Chichewa Kusamwerana madzi: Kudana kwambiri. Chitsanzo: Masiku ano samwerana madzi, akakumana sayankhulana. Kusamwetsa munthu madzi: Kusowetsa mtendere. Chitsanzo: Amene aja samwetsana madzi ndi apongozi awo. Kusandulika: Kusintha maonekedwe kapena zochita. Chitsanzo: (1) Anzathutu mwasandulikako kutauniku! (2) Yesu anasandulika atapita kukapemphera kuphiri. Kusanunkha kanthu: (a) Kudziona wachabechabe, osathandiza. Chitsanzo: Ife ndife osanunkha kanthu. (b) Zosathandiza, zochepa. Chitsanzo: Ndalama aperekanso sizinganunkhe kanthu. Kusanunkha kanthu: Mawuwa amanenedwa munthu ak- amadziderera kapena akamaderera winawake kuti ndi wosathandiza kapena wopanda ntchito. Chitsanzo: Ife ndiye ndi osanunkha kanthu. Kusanza madandaulo: Kunena madandaulo ako onse. Chitsanzo: Ndikupita kuofesi kwawo komweko kuti ndi- kasanze madandaulo anga. Kusaona bwino: Kukaikira munthu. Chitsanzo: Munthu amene uja sindimamuona bwino, ndi wokaikitsa. Kusasa fumbi: Umenewu ndi mwambo umene anthu a m’zikhalidwe zina amachita. Chimene chimachitika n’choti, tsikana akatha msinkhu kapena atangotsala pang’ono kutha msinkhu, amapita kuchinamwali ndipo kumeneko amakawalangiza kuti akayeserere kugonana ndi munthu. Ndiye amapeza munthu kuti agone naye. Chifukwa choti kamakhala koyamba, n’chifukwa chake mwambowu amautchula kuti kusasa fumbi. 186