Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 185
Paphata pa Chichewa
Kupyoza:
(a) Kubaya.
Chitsanzo: Nguluweyo anaipyoza ndi nthungo.
(b) Kuwawa, kupweteka.
Chitsanzo: Mawu amene anayankhula anandipyoza
mumtima.
Kusa: Kusonkhanitsa.
Chitsanzo: Anakusa azimayi onse kuti akawapatse
malangizo.
Kusagwira kwa mutu:
(a) Kusaganiza bwino, kusayenda bwino kwa mutu.
Chitsanzo: (1) Koma mutu wako ukugwira?
(b) Kusokonezeka, kusowa chochita.
Chitsanzo: Mutu wake sukugwira.
(c) Matenda a misala.
Chitsanzo: Mutu wake sumagwira.
Kusaimva: Kusalolera.
Chitsanzo: Atamva zoti amamunyoza, nayenso sanaimve
koma kumupitira komweko kuti akamutsire mphepo.
Kusakhazikika:
(a) Kumangoyendayenda.
Chitsanzo: Musandidalile, ndine wosakhazikika.
(b) Wopupuluma, obalalika.
Chitsanzo: Mayiwa ndi wosakhazikika.
Kusakwanitsidwa: Kusankhutira.
Chitsanzo: Galuyu ndi wosakwanitsidwa, wamaliza zake
akubweranso pano kuti amudyere nzakeyu.
Kusala:
(a) Kusadya kapena kusachitsa zinazake.
Chitsanzo: Ine ndimasala zakudya zimenezi.
(b) Kusakuwerengera, kukupatula.
Chitsanzo: Anthuwa amandisala.
184