Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 158

Paphata pa Chichewa Kulowerera: (a) Kuyamba kuchita makhalidwe oipa. Chitsanzo: Mwana uja analowerera. (b) Kupitira kutsogolo, kupita kukakhala kutsogolo n’kupitirira amene wawapeza. Chitsanzo: Mwana uyu amakonda kulowerera. Kuloweza: Kungozolowera kuti zimayenda chonchi. Chitsanzo: (1) Akumangoyendera kuloweza. (2) Analoweza kuti akabwera pano timamupatsa. Kuloza chala: Kuimba mlandu. Chitsanzo: (1) Ukasauka usaloze zala anzako omwe zikuwayendera. (2) Zikawavuta amayamba kuloza chala anthu ena. Kululuzika: Kuchita manyazi. Chitsanzo: Koma ndiye aluluzikatu! Akanadziwa sa- kanabwera. Kuluma khutu: Kuuza munthu nkhani yachinsinsi pang’ono. Chitsanzo: Upite kuti nawenso akakulume khutu. Kuluma mwala: Kulephera, kukumana ndi mavuto. Chitsanzo: Ukachita masewera uluma mwala. Kuluma nauzira: Mawuwa anachokera ku zimene khoswe amachita akamaluma chidendene kapena zala za munthu n’kuuzira kuti asamve kupweteka kwambiri. Angatan- thauze kupereka malangizo mwachikondi. Chitsanzo: Bambo awa amaluma nauzira. Kuluma pansi: Kugwa modetsa nkhawa. 157