Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 156
Paphata pa Chichewa
Kulowa chamutu: Kubwera kapena kuchita nawo
zinazake usanaitanidwe.
Chitsanzo: Awa sanaitanidwe, angolowa chamutu.
Kulowa chisawawa: Kuphweka, kumangochitidwa ndi ali-
yense.
Chitsanzo: (1) Ndinakana kusewera mpira chifukwa
zinangolowa chisawawa. (2) Bizinezi ya mandasi yan-
golowa chisawawa.
Kulowa khutu ili n’kutulukira lina: Kusamva.
Chitsanzo: Ukamuuza zinthu zimangolowa khutu ili n’ku-
tulukira linalo.
Kulowa kufa: Anthu ena amakhulupirira kuti bambo
akamwalira pakhomo, pamafunika kuti munthu wina
agone ndi mkazi wa munthuyo n’cholinga choti pakhomo-
po pasachitikenso tsoka lina. Miyambo ngati imeneyi ndi
imene ikukolezera moto kuti edzi ifale kwambiri.
Chitsanzo: Malirowa akangoikidwa, mpofunika kuchita
mwambo wa kulowa kufa.
Kulowa limodzi ndi nkhuku: Kugona mwachangu.
Chitsanzo: Anzanu aja amalowa limodzi ndi nkhuku.
Kulowa m’chala: Kumangodwaladwala.
Chitsanzo: Mayi awo alowa m’chala.
Kulowa m’mabuku: Kufufuza zambiri m’mabuku,
kuwerenga.
Chitsanzo: Kuti tipeze yankho ya funso limeneli mpo-
funika kulowa m’mabuku.
Kulowa m’madzi: Kuwonongeka, kusaoneka phindu lake.
Chitsanzo: Ndalama zanga zonse zangolowa m’madzi.
155