Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 150
Paphata pa Chichewa
ndikaphe mpola. (2) Ndikufuna ndikwawire kumudzi
kukaona matenda.
Kukwawa: Kuyenda pang’onopang’ono.
Chitsanzo: Chingolo chakechi chikungokwawa, tika-
nakhala titafika tikanayenda wapansi.
Kulabada: Kuwerengera, kulemekeza zomwe ena aku-
nena.
Chitsanzo: Salabada zoneneza za ena.
Kulaka: Kukanika.
Chitsanzo: Chalaka ameneyu palibe angachithe.
Kulakatika: Kukambidwa. Tanthauzo lenileni la mawuwa
amatanthauza kugwa pansi.
Chitsanzo: Nkhani zimene zimalakatika zinali zokhudza
kuipa kwawo.
Kulala: Kutha, kuzilala.
Chitsanzo: Moyo wathu ukulala ngati moto.
Kulandirira m’matumba obooka: Kulandira ndalama
n’kungopitirira.
Chitsanzo: Ndalama timangolandirira m’matumba obooka.
Kulanguluzika: Kuvutika.
Chitsanzo: Amasangalala akamationa tikulanguluzika
chonchi.
Kulaulidwa: Kuyankhulidwa kapena kuona zinthu zo-
chititsa manyazi.
Chitsanzo: Sindinaonepo zimenezi pamoyo wanga,
mwandilaula!
Kulavula mwano: Kunena mawu achipongwe kapena am-
wano.
149