Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 142
Paphata pa Chichewa
Chitsanzo: (1) Mfumu itamwalira, anthu onse samagwira
ntchito pokhudza maliro a mfumuyo. (2) Tikupita
kukakhudza maliro.
Kukhulula:
(a) Kungochita zinthu mpaka pamapeto.
Chitsanzo: Ndinamuuza kuti awerenge ndime imodzi, ko-
ma iye wangokhulula mpaka kumapeto.
(b) Kuchotsa ulusi umene unazengerezedwa, kusolola
ulusi pa chinthu, kumasula chingwe.
Chitsanzo: Wandikhululira juzi yanga.
Kukhuta ngati chubu: Kukhuta kwambiri.
Chitsanzo: Akakwiya amadya mpaka kukhuta ngati chubu.
Kukhutchumula:
(a) Kumenya.
Chitsanzo: Ukachita masewera akukhutchumula.
(b) Kutekesa chinthu mwamphamvu, kugwedezeka, ku-
menyetseka.
Chitsanzo: (1) Akukhutchumula thumba. (2) Akukhutchu-
mula botolo la mowa. (3) Galimotoyo imangotikhutchumu-
la.
Kukhuthura nkhawa: Kuuza wina mavuto ako onse.
Chitsanzo: Ndikufuna munthu woti ndimukhuthulire nkha-
wa zanga.
Kukhutira: Kukwanitsidwa ndi zimene uli nazo.
Chitsanzo: Kumakhutira ndi zomwe uli nazo.
Kukhuzumuka: Kudekha.
Chitsanzo: (1) Mmene akukulamu mpamene akukhuzu-
mukako, anali wovuta uyu! (2) Mwakhuzumukatu lero,
chachitika n’chiyani?
141