Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 140

Paphata pa Chichewa Kukhalira mphanthi: Kukhala movutika, mwamantha. Chitsanzo: Pakhomo pano tikungokhalira mphanthi. Kukhamukira: Kubwera m’chigulu. Chitsanzo: Onse anangokhamukira kunyumba kwanga. Kukhathamira: Kukwanira bwino. Chitsanzo: Ndiwozi zakhathamira ndi nsinjiro. Kukhetsa thukuta: Kugwira ntchito mwamphamvu, kugwira ntchito yowawa. Chitsanzo: Thukuta lonse lomwe ndinakhetsa langolowa m’madzi. Kukhiya: (a) Kumenya. Chitsanzo: Anzake akusukulu amukhiya. (b) Kufika pakolasi. Chitsanzo: Ndimavina koopsa nyimbo yake ikakhala yoti imadzikhiya. Kukhodola: Kusupula chinthu monga chilonda pogwiritsa ntchito chikhadabo. Chitsanzo: Ndinamupeza akukhodola zilonda. Kukhoma ndawala: Kuyenda mofulumira kwambiri. Chitsanzo: Ndakumana nawo atakhoma ndawala. Kukhoma: (a) Kumenya. Chitsanzo: Ndikukhomatu! (b) Kudzadza. Chitsanzo: Holoyo inakhoma ndi anthu. (c) Kumenya chinthu ndi chinachake. Chitsanzo: Akukhoma malata. 139