Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 129
Paphata pa Chichewa
(2) Mwana uyu ndi wogundika. (3) Ndinawapeza atagundi-
ka ndi kuba ndiwo.
Kugunyuza:
(a) Kukumbutsa.
Chitsanzo: Ndikakubwereka chinthuchi, ndisachite
kudzakugunyuza kuti udzabweze.
(b) Kugwedeza munthu kuti adzuke kapena akuyang’ane.
Chitsanzo: Tawagunyuzani akugonawo.
Kugupulira: Kulowerera nkhani ya eni.
Chitsanzo: Mwanayu amangogupulira nkhani za eni.
Kugwa chadodolido: Kugwa chagada, kugwa modetsa
nkhawa.
Chitsanzo: Anzanu aja anagwa chadodolido.
Kugwa khunyu: Kudwala matenda akugwa.
Chitsanzo: Mwanayu amagwa khunyu.
Kugwa m’chikondi: Kuyamba kukonda munthu kapena
chinthu china.
Chitsanzo: (1) Mnyamatayu wagwa m’chikondi ndi mtsi-
kana uja. (2) Ndagwa m’chikondi ndi filimu imeneyi.
Kugwa m’dothi: Kukula, kutha msinkhu.
Chitsanzo: (a) Ndinamufunsira asanagwe m’dothi. (b) Ana-
siya sukulu atangogwa m’dothi.
Kugwa m’papaya: Kusabereka.
Chitsanzo: Amene ajatu anagwa m’papaya, moti ndi
alonda chabe a akazi awo aja.
Kugwa majini: Kugwidwa ndi mizimu.
Chitsanzo: Pamaliro aja panali mayi wina yemwe anagwa
majini.
128