Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 126
Paphata pa Chichewa
Kugenda kupolisi chamba chili m’thumba: Kupalamula
ukudziwa kuti uli ndi mlandu kale.
Chitsanzo: Mwana ameneyu ofunika kumugwira n’ku-
mutsinatsina kuti asadzayambirenso kugenda kupolisi
chamba chili m’thumba.
Kugenda munthu ndi zam’kamwa: Kulavulira munthu
poyankhula kapena pakudya.
Chitsanzo: Musamayankhule pakudya mungatigende ndi
zam’kamwa.
Kugeza: Kusamba m’thupi.
Chitsanzo: Ndinamupeza akugeza.
Kugeza: Kusamba.
Chitsanzo: Ndikupita kumtsinje kukageza.
Kugodomala: Kupusa.
Chitsanzo: N’chifukwa chiyani nanunso muli ogodomala
chonchi!
Kugogoda:
(a) Kupweteka kumene kumamveka munthu akasenza
chinthu.
Chitsanzo: Chidebe ichi chimagogoda kwambiri,
sindingachisenze popanda nkhata.
(b) Kumenya chinthu.
Chitsanzo: Ndinamupeza akugogoda chitseko.
(c) Kumenya munthu.
Chitsanzo: Anzake ndi amene amugogoda.
Kugogomezera: Kutsindika mfundo kuti wina aimvetse.
Chitsanzo: Pofuna kugogomezera mfundoyo, anapereka
chitsanzo.
125