Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 120
Paphata pa Chichewa
kudzimanga. (2) Ntchito ngati za apolisi, zimafuna anthu
odzimanga.
Kudzimangirira: Kudzipha podzimanga ndi chingwe,
kudzikhweza.
Chitsanzo: Mwana wawo anadzimangirira.
Kudzimbuka: Kukwiya kwambiri mwadzidzidzi, kusintha
poyerayera.
Chitsanzo: Timacheza bwinobwino, koma titangotchula
nkhani imeneyi anangodzimbuka.
Kudzimva shuga (kudzimva uchi): Kuyerekedwa, kunya-
da.
Chitsanzo: Anthu akamamuyamikira amadzimva shuga.
Kudzimva: Kuyerekedwa, kunyada.
Chitsanzo: Bambo aja ndi wodzimva.
Kudzinyenga: Kudzinamiza, kudzipusitsa.
Chitsanzo: Ngati akuganiza kuti apambana akungodziny-
enga.
Kudzipachika (kupachikana): Kudziika pamavuto.
Chitsanzo: Apa ndiye mwadzipachikatu, zoona kuulula
nkhani yopusa ngati imeneyo!
Kudzipepesa: Kudya moti umveko bwino.
Chitsanzo: Ndagwira ntchito mwakhama, tsopano mpo-
funika kuti ndidzipepese.
Kudzipopa: Kuchita matama, kunena zambiri zokhudza
iweyo, kudzichemerera.
Chitsanzo: Mnyamata wake ndi wodzipopa, amangokha-
lira kunena zimene amachita.
119