Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 112
Paphata pa Chichewa
Kudushula: Kuchotsa.
Chitsanzo: Amudushula mutimu yawo.
Kuduwa: Amenewa ndi mawu achipongwe omwe achinya-
mata amagwiritsa ntchito ponena za munthu amene
wamwalira.
Chitsanzo: Akazi awo anaduwa.
Kudwala m’mimba: Kuda nkhawa.
Chitsanzo: Musatidwalitse m’mimba ndi nkhani zanu zon-
gopekazo!
Kudwala mwakayakaya: Kudwala kwambiri, kutsala
pang’ono kufa.
Chitsanzo: Achimwene awo akudwala mwakayakaya.
Kudya buku:
(a) Kuwerenga kwambiri.
Chitsanzo: Kuti ukhoze mayeso umafunika kudya buku.
(b) Kuphunzira kwambiri.
Chitsanzo: Munthu ameneyu anadya buku.
Kudya bwino:
(a) Kulemera, kukhala ochita bwino.
Chitsanzo: Banja ilo ndi lodya bwino.
(b) Kudya zakudya zabwino.
Chitsanzo: Ngakhale ali osauka koma amadya bwino.
Kudya chipwete cha lunda: Kutenga nthenga kwa akazi
kapena amuna.
Chitsanzo: Ndinakumana naye akuyenda tang’atang’a.
Zikuoneka kuti anadya chipwete cha lunda.
Kudya kakaka: Kuseka.
Chitsanzo: Ndinapeza aliyense akudya kakaka.
111