Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 105

Paphata pa Chichewa Kubwinyika: Kudya chonse nthawi imodzi. Chitsanzo: Ataona kuti timupempha anangobwinyika chonse. Kubwiza: Kudyetsa njomba. Mawuwa amakonda kugwir- itsidwa ntchito pochita masewera a mpira wa miyendo. Chitsanzo: Anabwiza wotseka kumbuyo n’kuchinya. Kuchapa: (a) Mawuwa amanenedwa mokokomeza ponena za mun- thu amene amamveka mwaphokoso akamadya. Chitsanzo: Achimwene anu ali m’nyumbamu, akuchapa. (b) Kumenya munthu koopsa. Chitsanzo: Anzake amuchapa. Kuchenjerera: Kuchitira wina zachinyengo, awatulukira. Chitsanzo: (1) Anzawo awachenjerera. (2) Amandiona nga- ti wogona, ndamuchenjerera. Kuchenuka: Kuzindikira, kuchangamuka. Chitsanzo: Ankangoti ndwii apa, lero achenuka akufuna atisowetse mtendere. Kuchenutsa: Kuchenjeretsa, kuthandiza munthu kuti akhale wozindikira. Chitsanzo: (1) Awa n’gofunika kuwachenutsa. Kucheukira: Kuthandiza. Chitsanzo: Ticheukireni achimwene, ifetu kuno usiwa. Tikungovala nsanza zokhazokha moti tikamayenda ziku- mangoti wirawira. Kuchikweza: (a) Munthu waluso, wotchuka komanso wolemekezeka. Chitsanzo: Malume aja ndi kuchikweza. 104