Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 103
Paphata pa Chichewa
Kubuka:
(a) Kutchuka kwambiri, kumveka.
Chitsanzo: Sindimadziwa kuti munthu amene uja angabu-
ke chonchi.
(b) Kuyambika.
Chitsanzo: (1) Nkhaniyi inabuka mwanayu atakadikiza
nsima kwawo. (2) Mavuto akabuka tizigwirana manja.
(c) Kuyaka.
Chitsanzo: Galimotozo zitangogundana, panabuka chimo-
to choopsa.
Kubulika:
(a) Kuyankhula mwano.
Chitsanzo: Usakadabwe pakamwa pake pakakayamba ku-
bulika phunzo.
(b) Kulawira kapena kudzuka mofulumira kwambiri.
Chitsanzo: Ndimadabwatu kuti zatani kuti abulike kusa-
nache?
(c) Kutuluka mofulumira kwambiri.
Chitsanzo: Mbewayo itaona kuti zavuta, inabulika. (2)
Mwamuna wakubayo anabulika m’nyumba atamva mawu
a mwini mkaziyo.
Kubushula: Kuchotsa mimba.
Chitsanzo: Atatenga mimba ali pasukulu, anangobushula.
Kubwadamuka: Kuwira.
Chitsanzo: Kodi madzi aja abwadamuka?
Kubwanyuka: Kuphwanyika.
Chitsanzo: Chimene anaumba chabwanyuka.
Kubwanyula: Kumenya.
102