Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 100
Paphata pa Chichewa
Chitsanzo: Achimwene, bwanji tipite paselipo tikabe
khonde.
Kuba tulo: Kugona. Nthawi zambiri amene amanena
mawuwa amakhala amene akufuna kugona pa nthawi
imene akugwira ntchito monga alonda.
Chitsanzo: (1) Kodi munali kuti, mumaba tulo? (2) Ndili
m’nyumbamu kaye, ndibe tulo.
Kubabalika: Kupupuluma.
Chitsanzo: Anzanuwa ndi obabalika.
Kubadwa: Kuyamba.
Chitsanzo: Dzina lakuti Nyasaland linabadwa pamene
azungu anamva zolakwika kwa munthu wina yemwe
ankalephera kumva chingerezi.
Kubaizika: Kusaganiza bwino, misala.
Chitsanzo: (1) Akukhala ngati wabaizika. (2) Munthu
ameneyu ndi wobaizika.
Kubaka: Kudya.
Chitsanzo: Ndangomaliza kumene kubaka nsima.
Kubaka: Kudya.
Chitsanzo: Ndawaona akubaka nsima.
Kubalalika: Kusokonezeka. Amatanthauzanso kumwa-
zikana.
Chitsanzo: Anzanuwa sachedwa kubalalika.
Kubanda:
(a) Kusokonekera mutu utasuta chamba.
Chitsanzo: (1) Chamba chamubanda.
(2) Akuoneka kuti wabandika.
(b) Kukusangalatsa, kukumaliza.
99