Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 7
Ngale
Anthu a m’mudzi wina amakonda kufotokozerana nkhani ya munthu wina
yemwe anapeza ngale yamtengo wapatali n’kuyitaya itamuwonetsa mavuto.
Dzina la munthuyu linali Kino, ndipo mkazi wake anali Juana. Banjali linali
ndi mwana m’modzi yemwe dzina lake linali Coyotito. Ndiye popeza nkhaniyi
yakhala ikukambidwa mobwerezabwereza, anthu anafika poyiloweza moti
amatha kuyinena ngakhale atadzidzimuka kutulo. Monga zimakhalira ndi
nkhani zomwe anthu akuzidziwa bwino, ndikulonjeza kuti sindichulukitsa gaga
kapena kubwitikiza madeya m’diwa. Ndingokufotokozerani ndendende mmene
zinachitikira.
Ngati nkhaniyi ili fanizo, aliyense apeze yekha tanthawuzo lake komanso awone
mmene ikukhudzira moyo wake. Imayamba motere . . .
Gawo 1
Kino anadzidzimuka kunja kusanachesetse. Nyenyezi zinali zikuwalabe
kuthambo ndipo zizindikiro zoti kunja kukucha zinali zitayamba
kuwonekera. Pa nthawiyi atambala anali atayamba kale kulira ndipo na-
zonso nkhumba zolawira zinkayendayenda m’madzala n’kumafufuza
chakudya chosadziwika chomwe chimazithandiza kuti zinenepe. Panja
pa nyumba ya Kino, yomwe tinganene kuti inali chisakasa chopangidwa
ndi mitengo komanso udzu, pankamveka kulira kwa mbalame zolawira
kotola mphutsi.
Pamene ankatsegula maso ake, Kino anawona kuwala komwe
kunkalowera m’nyumbayi kudzera m’mipata yomwe inali kukhomo
ndipo anayendetsa maso n’kuyang’ana bokosi lomwe munali mwana
wake, Coyotito. Kabokosiko kanamangiriridwa kudenga ndi zingwe
ziwiri ndipo kankalendewera m’malere. Kino anatembenukira mkazi
wake Juana, yemwe anagona pambali pake atafunda shawelo. Nthawi
zonse Kino akamadzuka ankapeza mkazi wakeyu akumuyang’ana. Kino
sankakumbukira tsiku limene anamuwonapo ali m’tulo.
Pamene m’maso mwake munkayera, anayamba kumva kulira kwa
mafunde omwe ankamenya m’mbali mwa gombe. Kino ankakhutira ndi
mmene zinthu zinkayendera pamoyo wake ndipo ankawona kuti zonse
zili tayale. Posakhalitsa anatsekanso maso ake n’kumamvetsera nyimbo
1