Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 63
Ngale
wanga! Undikhululukire pa zimene ndinakulakwirapo m’mbuyomu.”
Kenako anapumira pang’ono n’kunena kuti, “Ngati nditatsika anthuwa
n’kundiposa mphamvu, iweyo ungokhala chete. Sindikukayikira kuti
akagwira ineyo kapena kundipha atenga ngaleyi n’kubwerera. Zikatero
iweyo utsike n’kuthawira ku Loreto.”
Juana anali atagwira dzanja la mwamuna wakeyo ndipo atangomva
mawu amenewa anayamba malungo.
“Ndikuyenera kutero mkazi wanga,” anatero Kino. “Kupanda
kutero, mawa kukamacha atigwira ndipo tikhoza kufa imfa yowawa
zedi.”
Juana ankanjenjemera kwambiri tsopano, komabe anadzilimbitsa
n’kunena kuti, “Mulungu akutsogolereni.”
Kino anayang’ana mkazi wakeyo kwa kanthawi. Zina zimangochi-
tika, koma kunena zowona anthuwa ankakondanadi, kaya pamavuto
kapena pamtendere. Aliyense anali wokonzeka kupereka moyo wake
kuti apulumutse banja lake. Kino anayendetsa dzanja lake n’kusisita
mwana wake Coyotito. Kenako nkhope yake itakutidwa ndi chisoni,
anagwira mwachikondi tsaya la mkazi wakeyo. Zinali zolilitsa zedi.
Posakhalitsa Juana anawona Kino akuvula malaya ake oyera aja.
Imeneyi inali nzeru chifukwa thupi lake lachimwenye likanamuteteza
kusiyana ndi malaya oyerawo, omwe ankawonekera patali kwambiri.
Juana anawona mwamuna wakeyo akukoleka chingwe cha mpeni
wawukulu uja m’khosi ndipo mpeniwo anawuberekera kumbuyo. Zime-
nezi zinachititsa kuti manja ake onse azigwira ntchito zina. Atangotulu-
ka n’kusiyana ndi mkazi wakeyo sanabwererenso. Juana ankangow-
onerera mwamuna wakeyo akupita ku Gologota kukapachikidwa ndipo
palibe chimene akanachita.
Coyotito anali atagona. Zimenezi zinapereka mpata kwa Juana kuti
azipempherera mwamuna wake kuti Mulungu amuteteze.
Kino anayamba kutsetsereka pang’onopang’ono kuchokera panali
mapanga paja. Iye ankakwawa mpeni wake uli kumbuyo ndipo izi zi-
nathandiza kuti usachite phokoso pomenya mwalawo n’kumugwiritsa.
57