Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 57
Ngale
wake kuja. Iye ankadziwa kuti anthuwo sangalephere kuzindikira kuti
pamalowo pali anthu, makamakanso akawona kuti wina amayesa
kufufuta mapazi ake ndi nthambi yamtengo. Anthuwa sanali oti unga-
wapusitse. Choncho Kino ankafuna kuti anthuwo akangofika pamene
ankafufuta mapazi paja, awawukire. Iye ankalakalaka atalumphira
munthu anali pahatchi uja. Ankadziwa kuti kusokoneza ameneyu
kungachititse kuti enawo akhale opanda mphamvu. Cholinga chake chi-
nali kulanda mfuti n’kuyigwiritsa ntchito polanga enawo. Pamene
anthuwo ankayandikira, Kino anakonzekera kuti awajowere.
Posakhalitsa Juana anamva kulira kwa hatchi. Pa nthawi imeneyi
Coyotito anali akuchita phokoso chapansipansi. Mwansanga, Juana ana-
munyamula mwana wakeyo n’kumutseka pakamwa.
Ofufuza mapazi aja atayandikira, Kino ankangowona mapazi a
anthu awiri aja komanso a hatchi ija. Anthuwa anavala nsapato zakutha
komanso mabuluku othimbirira. Kenako Hatchi ija inayima n’kuyamba
kuyendetsa mutu wake kwinaku ikulira. Nthawi yomweyo ofufuza
mapaziwo anatembenuka n’kuyang’anitsitsa makutu a hatchiyo kuti
awone ngati yazindikira kuti penapake pabisala anthu.
M’mimba mwa Kino munabwadamuka ndi mantha. Kwa nthawi
yayitali anthuwo ankangoyang’ana munsewu muja koma sanawone
chizindikiro chogwira mtima chamapazi a anthu. Kenako anapitiriza
ulendo wawo akuyang’ana mosamala munsewumo. Munthu anali pa-
hatchi uja anapitirizabe kuyenda pambuyo pawo. Mtima wa Kino una-
khalako pansi. Komabe, ankadziwa kuti mavuto akadalipo. Sankaka-
yikira kuti anthuwo akhoza kubwereranso.
Anthu aja atangotha kamtunda pang’ono, Kino anadzambatuka
n’kulowera kumene kunali mkazi wake. Ulendo uno sanavutike ndi
kufufuta mapazi ake. Ankadziwa kuti pali kale zizindikiro zambirimbiri
zimene zingawagwiritse. Timitengo tambirimbiri tinali titathyoledwa
ndi mapazi awo, ndipo timiyala tina tinali titasuntha chifukwa chaku-
lemera kwa matupi awo. Kino anayamba kuchita mantha kwambiri.
Ankadziwiratu kuti akhoza kugwidwa. Posakhalitsa anafika pamene
panali Juana akuchita befu ndipo mkazi wakeyo ankangomuyang’ana
ndi nkhope yamafunso.
51