Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 48
Ngale
munthu woti amuyimbire mtiwiso n’kumuwuza kuti masiku akale aja
sadzabwereranso. Thupi la munthu wosadziwikayo komanso mpeni
wamagaziwo zinalanduliratu kuti moyo wawo sudzabwereranso mwa-
kale. Iye anazindikira kuti chomwe akufunika kuchita tsopano ndi kupu-
lumutsa banja lake.
Zowopsa zimene anawonazi zinachititsa kuti ululu ankamva
patsaya komanso pamwendo wake uja ubalalikiretu. Mofulumira anag-
wira miyendo ya munthu wakufayo n’kuyamba kumukokera patchire.
Atachoka kumeneko anapita pamene panali Kino n’kukayamba ku-
mupukuta chipumi chake chatsoka chija, chomwe chinawumbudzid-
wanso mwankhanza. Juana anapukuta magazi omwe ankatuluka pachi-
pumipo ndi siketi yake.
“Basitu atenga ngale ija. Ngale ija yapita Juana,” anatero Kino
modandawula.
“Usadandawule mwamuna wanga. Palibe amene watenga ngale
yathu. Ili ndi ineyo. Ndayipeza pansi pa mwala m’mbali mwa njirayi.
Koma mukumva zimene ndikunenazi? Ngale yathu sinatengedwe,” ke-
nako anayang’ana mpeni uja n’kunena kuti, “Koma tawonani mwapha
munthu! Tiyeni tithawe mwansanga anthu angatigwire n’kutipha. Tiyeni
tithawe dzuwa lisanatuluke.”
“Komatu anachita kundiwukira. Nanga ine ndachita kukamupeza
pakhomo pake ngati?” anatero Kino. “Ndamupha podziteteza.”
“Mwakumbukira zimene zinachitika dzulo zija?” anafunsa Juana.
“Mukuganiza kuti pali amene angamvetsere zimenezo? Mwakumbukira
zimene ogula ngale aja anachita? Mukuganiza kuti zingakhale zomveka
titawawuza zimenezi ndi chakukhosi chimene akutisungira chifukwa
chowakaniza kuwagulitsa ngaleyi?”
“Sizingamvekedi,” anatero Kino. “Ukunena zowona Juana.” Mtima
wake unali utalimbanso tsopano. Iye anali atasandukanso munthu wam-
wamuna.
“Pita kunyumba ukatenge mwana,” anatero Kino. “Ukatengenso ufa
wonse womwe tili nawo. Ineyo ndithamange ndikayambe kukankha
bwato lathu. Chita machawi, undipeza kudoko.”
42