Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 41
Ngale
Ena ankanena kuti Kino walakwitsa kwambiri pokana kulandira
1,500 pesos. Ankawona kuti imeneyo ndi ndalama yochuluka yomwe
pamoyo wake sanayigwirepo. Gulu la anthu amenewa linkawona kuti
Kino wataya bomwetamweta. Ena ankadzifunsa kuti, ‘Kodi Kino
walimbadi mtima kupita kumzinda wawukulu kuti akagulitse ngale
yakeyo?’
Winanso ananena mwamantha kuti, “Ogula ngale ajatu amukwiyira.
Ndikuwona kuti sangalolenso kumugula, moti akasowa koyigulitsa.
Wangodziwonongera msika basi.”
Enanso ankati, “Kino ndi munthu wanzeru ndipo wachita bwino
osawagulitsa ngaleyo. Zimene wachitazi zitithandiza tonsefe.”
Kino anakhala m’nyumba mwake muja n’kumaswa mutu. Pa nthaw-
iyi n’kuti atabisa ngale yake ija pansi pa mwala pafupi ndi pamene
ankakoleza moto paja. Kino anali ndi mantha. Iye anali asanachokepo
kwawoku n’kupita kwina. Chinthu chinanso chomwe chinkamudetsa
nkhawa chinali choti mzinda wawukuluwo unali kutali zedi. Munthu
ankafunika kuwolola nyanja komanso kudutsa mapiri ambirimbiri.
Choncho akaganizira kutalika kwa ulendowu, mphamvu zinkamuthera.
Komabe, iye ankadziwa kuti akufunika kuchita zinthu mwachamuna
ngati akufuna kuti zimuyendere. Iye sakanalola kuti maloto okhudza
tsogolo lake asokonezedwe ndi winawake.
“Inetu ndikapondako kumeneko,” ananena zimenezi motsimikiza
mtima. Ankakhulupirira kuti chilichonse ndi chotheka bola ngati mun-
thu walimba mtima.
Pamenepa mpamene Juan Tomas anatulukira ndipo anakhala pam-
bali pa Kino. Chifukwa chosamvetsa zimene zinachitika m’mawa uja,
Juan Tomas sanayankhule kwa nthawi yayitali. Koma kenako Kino anati:
“Koma nanga ndikanatani? Anthu ajatu amafuna kungondibera!”
Juan Tomas anagwedezera mutu. “Timadziwa kuti alendo amenewa
amangotilima pansana komanso kutidyera masuku pamutu. Amatigu-
litsa zinthu zawo modula kwambiri ndipo eni nthakafe timazunzika
kowopsa mpaka kumwalira. Koma ndikuwuze pano m’bale wanga, kun-
jaku kunayanja lichero. Walakwitsa kwambiri kuwakaniza kugula ngale
35