Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 32
Ngale
“Kodi mukuwopa ndani?” anafunsa Juana.
Kino anayamba kufufuza yankho m’mutu mwake, ndipo atalipeza
anati: “Aliyense.”
Usiku umenewo Juana sanasiye mwana wake m’bokosi ankamu-
goneka lija powopa kuti angalumidwenso ndi pheterere wina. Anango-
mufukata m’manja mwake. Patapita nthawi, moto ankaphikira uja
unazima ndipo m’nyumbamo munangotsala mdima wokhawokha.
Usiku umenewo, Kino analota maloto. M’malotowo, Coyotito anali
atayamba sukulu ndipo ankawerenga buku lalikulu ngati nyumba.
Bukulo linali ndi zilembo zazikulu ngati agalu ndipo zilembozo zin-
kathawa m’bukumo moti posakhalitsa masamba ake ankangowoneka
mdima wokhawokha. Mdima umenewo unabweretsa nyimbo yoyipa
m’mutu mwa Kino ndipo chifukwa cha mantha, anadzidzimuka.
Atamvetsera mwatcheru mumdima wawusikuwo, Kino anazindikira
kuti chinthu chinachake chinkayenda nyumbayo chakukona kuja. Iye
anaduliratu mpumo kuti amve kalikonse. Zikuwoneka kuti nachonso
chinthu chinali mumdimacho chinali chitayima kaye n’kumamvetsera.
Kwa kanthawi sipanamvekenso phokoso lililonse. Koma kenako pho-
kosolo linayambiranso.
Kino anapisa nkono wake m’malaya n’kutulutsa mpeni ndipo atan-
gotero anadzambatuka ngati nyalugwe n’kulumphira kukona kuja. Ku-
meneko anakhudza munthu ndipo ataponya dzanja lake kuti amubaye,
anamuphonya. Keneko anaponyanso dzanja lake ndipo anamusosola na-
wo. Mwadzidzidzi anangomva chinachake chamung’amba chipumi.
Ululu umene anamva pamenepo unali wosaneneka moti anagwera pansi
ndipo munthu uja anapezerapo mwayi n’kuthawa. Pambuyo pa zimene-
zi kunja kunangoti chu-u!
Kino ankatha kumva magazi otentha akuyenderera pachipumi
chake. Ankamvanso Juana akumuyitana. “Kino! Kino!” Juana ankayitana
mwamantha zedi chifukwa anamva phokoso lonse la kukunthana kuja.
Pa nthawiyi Kino anali ndi mantha aakulu. Iye sankafuna kuti mkazi
wakeyo adziwe zimenezi moti anamuyankha kuti, “Usadandawule ndili
bwinobwino. M’nyumba muno munalowa wakuba.”
26