Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 25
Ngale
ena ankanong’onezana kuti, “Mfuti. Akuti agula mfuti.”
Pamene nyimbo ya ngale inkamveka kwambiri m’mutu mwa Kino,
Juana anatukula mutu wake. Nkhope yake inali itawala ndi chisangalalo
pozindikira zinthu zanzeru zimene mwamuna wake ankafuna kuchita
akagulitsa ngaleyo. Tsopano Kino akanatha kuchita chilichonse chimene
akufuna. Dziko lonse linali m’manja mwake tsopano. Iye akanatha ku-
tumiza mwana wake kusukulu kuti akadye bukhu. Kino anayang’ana
anthu aja mokhala ngati watulukira mfundo yofunika kwambiri ndipo
anati, “Mwana wanga adzapita kusukulu, mwana wanga adzakhala
wophunzira.” Mtima wa Juana unalumpha ndi chisangalalo ndipo
anayamba kuyang’ana mwana wake asakukhulupirira kuti zimenezo
zingachitikedi.
“Mwana wanga adzaphunzira kuwerenga ndi kulemba ndipo
azidzatsegula mabuku. Ndikukuwuzani kuti mwana wanga adziwa ku-
lemba ndi kuwerenga. Aphunziranso kuwerengera masamu ndipo nzeru
zimene atapeze kusukuluko zidzathandiza tonsefe kuti titseguke
m’maso. Mwana wanga akaphunzira, ndiye kuti tonse taphunzira.” Aka-
yang’ana ngale ija, Kino ankatha kudziwona ali ndi mkazi wake, atakha-
la m’kanyumba kawo kabwino akuwothera moto, Coyotito ali pambali
pawo akuwerenga nzeru zobisidwa m’mabuku.
“Ndikagulitsa ngaleyi ndichita zimenezi,” anatero Kino. Koma ke-
nako chinachake chinamuwuza kuti pakamwa pakepo pakhoza kumuyi-
ka m’mavuto. Ankadziwa bwino mwambi wakuti bongololo sadzolera
mafuta pagulu. Ngati pali khomo lomwe limachititsa kuti munthu awo-
nongeke, ndiye ndi pakamwa. Kino anazindikira mfundoyi mochedwa
moti anafumbata ngale yake n’kutseka pakamwa.
Kunja kunali kutatsala pang’ono kuda ndipo Juana anapita
kukasonkha moto. Alendo aja atawona kuti dzuwa lalowa anazindikira
kuti nthawi yoti abalalikire m’makwawo yakwana. M’modzim’modzi
anayamba kufumuka, koma ankachita zimenezi monyinyirika.
Posakhalitsa moto unakolera ndipo m’nyumba monse munayamba
kuwala. Pamene Juana ankati azitereka nkhali, anangomva anthu aku-
ponyerana mawu akuti, “Wansembe akubwera. Bambo Mfumu
akubwera!”
19