Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 14

Ngale Kino ndi Juana akudutsa. Tisanameyi, opemphapemphawa anali ana- mandwa pa nkhani zamakobidi komanso mitengo ya zinthu moti atangowona siketi ya Juana komanso shawelo yobowokabowoka yomwe anaberekera mwana wake, komanso bulangete lakutha la Kino ndi zovala zake zoperepeseka chifukwa chochapidwa kwambiri, sanaka- yikire kuti anthuwa ndi amphawi adzawoneni. Kunena zowona, opemphapemphawa ankadziwa chilichonse chom- we chinkachitika m’tawuniyi. Popeza ankagona panja pa tchalitchicho, iwo ankadziwa anthu onse omwe ankabwera kudzalapa machimo awo kwa wansembe. Palibe amene ankalowa n’kutuluka m’tchalitchimo iwowa osadziwa. Komanso ankadziwa bwino dokotala uja. Ankadziwa kuti doko- talayo ndi munthu woyipa mtima zedi komanso kuti akhoza kuchita chilichonse kuti apeze khobidi. Ankadziwanso nkhanza zake, kuchuluka kwa machimo ake omwe anawunjikana mpaka kumwamba komanso azimayi osawerengeka omwe anawathandiza kuchotsa mimba. Iwo ankadziwa bwinobwino kuti dokotalayo ankagwira ntchito yotamandi- ka zedi pa nkhani yotumiza anthu kumwamba, kapena ku Gehena, masiku awo asanakwane. Opemphapemphawa anali atatopa ndi kuwona mitembo yosawerengeka yomwe inachoka m’manja mwa doko- talayu n’kubwera kutchalitchiku isanapite kukayikidwa. Ndiye popeza kutchalitchiku kunalibe anthu, nawonso anatsatira chitsinda cha anthu chija. Ankafunitsitsa kuwona zimene dokotala wadyerayo angachite ndi mwana wa munthu wochakachikayo. Posakhalitsa gulu la anthulo linafika pakhomo lolowera kumpanda wa dokotalayo. Anthuwo ankatha kumva kafungo ka zakudya zabwino- zabwino zomwe zinkaphikidwa kumpandako. Kino anakayikira kwa kanthawi asanagogode. Chomwe chinkamuwumitsa nkono ndi choti do- kotalayu sanali wamtundu wake. Anali wamtundu wina, womwe kwa zaka pafupifupi 400 unkangokhalira kuzunza komanso kubera anthu a mtundu wa Kino. Chimenechi n’chifukwa chake mtima wake unkamu- wawa kwambiri akawona anthu a mtunduwu. Ndi zimenenso zinachi- tika patsikuli moti Kino sankafuna ngakhale kuyankhula naye. Ko- manso, anthu amtundu wa dokotalayo anali aphunzo. Akamayankhula 8