Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale | Page 10

Ngale lake lija. Kenako anayamba kupesa tsitsi lake n’kulimanga kumbuyo ndi maliboni obiriwira. Kino ananjuta pafupi ndi moto n’kumadya mikate yake. Atamaliza kudya, anatenga kapu ya madzi n’kumwera. Juana nayenso anabwera n’kudya mikate yake. Chichereni, anthuwa anali atangoyankhulana kamodzi kokha basi. Iwo sankawona chifukwa cho- mangokhalira kukamwa mbe-e ndi nkhani zosafunika kwenikweni. Nthawi zambiri ankangoyankhulana ndi maso. Kino anapuma mwam- phamvu ndipo ichi chinali chizindikiro choti wakhutira ndi zimene mka- zi wakeyo wachita. Onse ankawoneka osangalala. Tsopano dzuwa linayamba kukwera moti kuwala kwake kunadutsa m’ming’alu komanso mipata ing’onoying’ono ya nyumba ya Kino. Ku- walako kunkangokhala ngati mapayipi ataliatali m’nyumbamo ndipo kwina kunalunjikanso pabokosi la Coyotito komanso pazingwe zomwe zinamangiriridwa kudenga zija. Kuwala kumeneku n’kumene kunathan- diza Kino ndi Juana kuwona chinthu china chomwe chinkayenda pachingwe chimodzi cha bokosilo. Thupi la Kino ndi Juana linangowumiratu atawona chinthucho. Mmene chinkayendera, zinali zowonekeratu kuti ndi pheterere. Kino anapuma mwaphokoso zedi chifukwa chankhawa ndipo po- funa kuti phokoso la mpumowo lisadzidzimutse pheterereyo, anayamba kupumira mkamwa. Kenako anapitirizabe kuyang’ana pheterereyo thupi lake litawuma ngati mtembo. M’maganizo mwake munali mutayamba kumveka nyimbo yachilendo. Imeneyi inali nyimbo yoyipa, nyimbo ya mdani, nyimbo yowopsa. Nyimbo ya Banja Lake ija inali itasiya kulira. Pheterereyo anatsetserekabe ndi chingwecho mchira wake uli m’mwam- ba. Juana anayamba kupemphera chapansipansi. Iye ankapempha mi- lungu yamakolo ake kuti ithamangitse tsokalo. Kuwonjezera pamenepa, ankayitananso Mariya Woyera kuti ateteze mwana wakeyo. Ankachita izi posadziwa kuti chipulumutso chichokera kuti. Pa nthawi imeneyi Ki- no anayamba kuyenda ngati akuponda pamoto n’kumalowera kunali bo- kosi kuja. Maso ake anangoti ga pa pheterereyo. Koma zimene zimachi- tika nthawi zina zimakhala kamba anga mwala. Zimene Coyotito anachi- ta pamenepa zinali zoti sungaziyembekezere. Zoti makolo ake anali akugwa ndi mapemphero powopa pheterereyo analibe nazo ntchito. 4