Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale 2 | Page 40
Ngale
Kino anapsa mtima atamva zimenezi moti anamukwatula ngaleyo
n’kuyiyikanso pakansanza kaja.
Munthu wonenepa uja anayambanso kuyankhula ndipo anati,
“Wawonatu mnzanga! Ndakupatsa mtengo wabwino zedi. Palibenso
kwina kumene ungakagulitse ngale imeneyi pamtengo wongopereka
ngati umenewu. Ndiye ukuti bwanji? Ndikupatse 1,000 pesos yako uz-
ipita? Sindikuganizanso kuti uchita bobobo pamenepa chifukwa
ukatero, ukhoza kunong’oneza bondo pamapeto pake!” anatero pamene
Kino ankayika ngale yake m’thumba la malaya.
“Ndinu anthu akuba kwabasi,” anatero Kino mokwiya. “Ndikhoza
kungotayapo nthawi pano. Ndipita kukagulitsa ngale yangayi kumzinda
wawukulu.”
Tsopano ogula ngalewo anazindikira kuti mwayi wogula ngale
yamtengo wapataliyo wawapulumuka m’manja moti munthu wonenepa
uja anawonjezera mtengo ananena poyamba uja. Iye anati: “Chabwino,
ndikugula 1,500.”
Koma pamene ankanena zimenezi, Kino anali atatuluka kale panja.
Pamene ankadutsa pakati pa gulu lomwe linali panjapo, anamva anthu
akuyankhula zinthu zosiyanasiyana koma sanawasamale. Juana anamut-
satira pambuyo pake chothamanga.
Madzulo a tsiku limenelo, anthu oyandikana nawo nyumba aja
analowa m’nyumba zawo n’kumadya mikate yawo. Iwo ankakambirana
zimene zinachitika m’mawa wa tsikulo. Kunena zowona, nawonso anali
asanawonepo ngale yayikulu ngati ya Kino ndipo ankadziwanso kuti
ogulawo anali akatswiri pa nkhani yonena kuti ngale iyi ndi yabwino
kapena ayi.
“Ine ndikuwona kuti ogula aja sanachite kupangana kuti anene mi-
tengo imene ija,” ankatero anthuwo. “Onse atatu amawona kuti ngale ija
ndi yopanda ntchito.”
“Koma mwina amanama! Ndani akudziwa, mwina anagundana mi-
tu! Pajatu apawo ndi mizu ya kachere, amakumana pansi.”
“Komatu ngati zilidi zowona ndiye kuti amangotibera tikamawagu-
litsa ngale zathu.”
34