Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale 2 | Page 35
Ngale
pambuyo ngati ngolo, kunsana kwake atabereka Coyotito. Kenako
analunjika nsewu wopita m’tawuni ndipo anthu a nyumba zapafupi aja
anawatsata mwawunyinji. Ndiye popeza tsikuli linali lofunika zedi,
pambali pa Kino panali mchimwene wake, Juan Tomas.
“Usakachitetu zogona anthu ake ndi akuba. Zingakhale zomvetsa
chisoni kwambiri ngati atakakunenerera mpaka kukugula pamtengo
wolira,” anatero Juan Tomas.
“Zowonadi, anthu amenewa ndi amambala kwabasi,” anavomereza
Kino.
“Sitikudziwa kuti m’madera ena anthu amagulitsa ngale pamitengo
yotani,” anatero Juan Tomas. “Nanga tingadziwe bwanji ngati ogula
ngale akunowa amatigula pamitengo yabwino? Ndimalakalaka tsiku
lina nditazadziwa mitengo yomwe amawagula kumene amakagulitsako
akatigula ifeyo kunoko.”
“Zowonadi,” anatero Kino, “koma nanga tingadziwe bwanji ngati
pali amene anayamba wachokapo kuno n’kupita m’matawuni ena?”
Pamene ankayenda, khamu la anthu linkawatsatira lija linkangokuli-
rakulira. Atawona khamuli, Juan Tomas anayamba kuchita mantha
ndipo anati:
“Iweyo usanabadwe Kino,” anayamba motero Juan Tomas,
“akuluwakulu amtundu wathu anapeza njira yoti azigulitsa ngale zawo
pamitengo yabwino. Anaganiza zopeza munthu woti atenge ngale zonse
n’kukazigulitsa kumzinda wawukulu.”
“Ndinamvadi zimenezo,” anatero Kino. “Ndimawona kuti analinga-
lira bwino kwambiri.”
“Posakhalitsa anapezadi munthu n’kumupatsa ngale zawozo,”
anapitiriza Juan Tomas, “Koma munthuyo atangochoka kuno, sanabw-
ererenso. Kungochokera tsiku limenelo palibe anamvanso za iye.
Zimamveka kuti achifwamba ndi amene anamupotokola khosi
n’kutenga ngale zonse. Patapita nthawi anatumizanso wina, ndipo atan-
gochoka kuno, nayenso sanawonekenso. Atawona kuti njirayi itha anthu,
anangoganiza zobwerera ku njira yakale ija.”
29