Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Ngale 2 | Page 33

Ngale Kenako anayamba kupapasapapasa akubwerera kunali mphasa ku- ja. Juana anali akukoleza moto kuti m’nyumbamo muwale. Atangowona bala lomwe linali pachipumi chamwamuna wakeyo, anaviyika nsanza m’madzi n’kuyamba kumupukuta. “Zazing’ono zimenezi,” anatero Kino modzilimbitsa mtima, maso ake akuwoneka mowopsa. “Ngale imeneyi ndi yoyipa mwamuna wanga,” anatero Juana. “Tiyeni tingoyitaya. Tikachedwa ikhoza kutiwonongera banja lathu.” Ndi kuwala kwa moto anakoleza uja, Kino ankatha kuwona maso a Juana atangotsala pang’ono kufwamphuka m’chimake chifukwa cha mantha. Koma Kino sanamvere zonena za mkazi wakezi. “Umenewu ndi mwayi wathu Juana,” anatero Kino. “Mwana wathu akufunika kudzapi- ta kusukulu. Ayenera kuphunzira kuti asadzavutike ngati ifeyo. Kapena- tu iwe sukufuna?” “Koma ayi Kino, ngaleyi itipweteketsa,” anatero Juana. “Ikhozanso kupweteketsa mwana wathuyu.” “Basi khala chete,” anayankhula mozazira Kino. “Mawa tikagulitsa ngaleyi, ndipo masokawa atichoka. Zinthu zibwereranso mwakale.” M’maso mwa Kino munkawoneka kuwala kwa moto uja. Pa nthawiyi mpamene anazindikira kuti mpeni uja unali udakali m’manja mwake. Atawona kuti uli ndi magazi, anawubayitsa pansi kuti achoke. Tsopano unali m’bandakucha ndipo Kino anasuntha mphasa n’kufu- kula ngale ija. Kenako anayamba kuyiyang’ana mwachidwi. Ngaleyo inkawala ndi malawi a moto uja. Kunena zowona inali yokongola zedi komanso yosalala bwino moti atayiyang’ana, anayamba kumva nyimbo m’mutu mwake. Inali nyimbo yachisangalalo komanso yatsogolo lowala. Nyimboyi inachititsa kuti Kino ayambe kumwetulira mosadziwa. Popeza maso alibe mpanda, diso la Juana linaphuluza n’ku- muwona akusekerera. Ndiye popeza mwamuna ndi mkazi okwatirana ndi thupi limodzi, nayenso anagwirizana ndi mwamuna wake n’ku- mamwetulira naye limodzi. Ngakhale Kino anavulazidwa ndi wakuba uja, zikuwoneka kuti tsikuli analiyamba ndi chiyembekezo. 27